Mmodzi mwa amene anamenyela ufulu wa Mozambique bambo Chuzombo wapempha chipani cholamula boma cha Frelimo ndi chipani chotsutsa boma cha Renamo kuti athetse ziwembu zimene zikuchitika mdzikomo. Mtola nkhani wathu Bright Sonjera walankhula ndi mkuluyu. Boma la Malawi layamba kupeleka zitupa kwa nzika zake kuti mbiri ya munthu aliyesne ikhale mu nkhokwe ya dzikolo. Maiko ambiri amu Africa anapanga kale zimenezi. Martina Mlelemba akusimba. Pano tiyeni tikumane ndi Tina Nyirenda ndi nkhani za masewera. Maboma a Malawi ndi Mozambique agwilizana zakhwimitsa nchito yakulimbana ndi mchitidwe wakupha malubino.